Ezara 2 (CCL)

Mʼndandanda wa Ayuda amene Anabwerera
1Awa ndi anthu a mʼchigawo cha Yuda amene anabwerako ku ukapolo, amene Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni anawagwira ukapolo ndi kupita nawo ku Babuloni (iwo anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense ku mzinda wake. 2Iwo anabwerera pamodzi ndi Zerubabeli, Yesuwa, Nehemiya, Seruya, Reelaya, Mordekai, Bilisani, Misipara, Bigivai, Rehumu ndi Baana).
Chiwerengero cha anthu aamuna a Israeli chinali chotere:
3Zidzukulu za Parosi2,172
   4zidzukulu za Sefatiya372
   5zidzukulu za Ara775
   6zidzukulu za Pahati-Mowabu (zochokera kwa Yesuwa ndi Yowabu)2,812
   7zidzukulu za Elamu1,254
   8zidzukulu za Zatu945
   9zidzukulu za Zakai760
   10zidzukulu za Bani642
   11zidzukulu za Bebai623
   12zidzukulu za Azigadi1,222
   13zidzukulu za Adonikamu666
   14zidzukulu za Bigivai2,056
   15zidzukulu za Adini454
   16zidzukulu za Ateri (kudzera mwa Hezekiya)98
   17zidzukulu za Bezayi323
   18zidzukulu za Yora112
   19zidzukulu za Hasumu223
   20zidzukulu za Gibari95.
21Anthu a ku Betelehemu123
   22Anthu aamuna a ku Netofa56
   23Anthu aamuna a ku Anatoti128
   24Anthu aamuna a ku Azimaveti42
   25Anthu aamuna a ku Kiriati Yearimu, Kefira ndi Beeroti743
   26Anthu aamuna a ku Rama ndi Geba621
   27Anthu aamuna a ku Mikimasi122
   28Anthu aamuna a ku Beteli ndi Ai223
   29Anthu aamuna a ku Nebo52
   30Anthu aamuna a ku Magaibisi156
   31Anthu aamuna a ku Elamu wina1,254
   32Anthu aamuna a ku Harimu320
   33Anthu aamuna a ku Lodi, Hadidi ndi Ono725
   34Anthu aamuna a ku Yeriko345
   35Anthu aamuna a ku Sena3,630.
36Ansembe anali awa:
   Zidzukulu za Yedaya (kudzera mu banja la Yesuwa)973
   37Zidzukulu za Imeri1,052
   38Zidzukulu za Pasuri1,247
   39Zidzukulu za Harimu1,017.
40Alevi anali awa:
   Zidzukulu za Yesuwa ndi Kadimieli (kudzera mwa ana a Hodaviya)74.
41Anthu oyimba nyimbo anali awa:
   Zidzukulu za Asafu128.
42Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali awa:
   Zidzukulu za Salumu, zidzukulu za Ateri, zidzukulu za Talimoni, zidzukulu za Akubu, zidzukulu za Hatita ndi zidzukulu za Sobai139.
43Otumikira ku Nyumba ya Mulungu anali awa:
Zidzukulu za
   Ziha, zidzukulu za Hasufa, zidzukulu za Tabaoti,
   44zidzukulu za Kerosi, zidzukulu za Siyaha, Padoni,
   45zidzukulu za Lebana, zidzukulu za Hagaba, zidzukulu za Akubu,
   46zidzukulu za Hagabu, zidzukulu za Salimayi, zidzukulu za Hanani,
   47zidzukulu za Gideli, zidzukulu za Gahari, zidzukulu za Reaya,
   48zidzukulu za Rezini, zidzukulu za Nekoda, zidzukulu za Gazamu,
   49zidzukulu za Uza, zidzukulu za Peseya, zidzukulu za Besai,
   50zidzukulu za Asina, zidzukulu za Meunimu, Nefusimu,
   51zidzukulu za Bakibuku, zidzukulu za Hakufa, zidzukulu za Harihuri,
   52zidzukulu za Baziruti, zidzukulu za Mehida, zidzukulu za Harisa,
   53zidzukulu za Barikosi, zidzukulu za Sisera, zidzukulu za Tema,
   54zidzukulu za Neziya ndi zidzukulu za Hatifa.
55Zidzukulu za antchito a Solomoni zinali izi:
Zidzukulu za
   Sotai, zidzukulu za Hasofereti, zidzukulu za Peruda,
   56zidzukulu za Yaala, zidzukulu za Darikoni, zidzukulu za Gideli,
   57zidzukulu za Sefatiya, zidzukulu za Hatilu,
   zidzukulu za Pokereti, Hazebayimu ndi Ami.
   58Chiwerengero cha onse otumikira ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi zidzukulu za Solomoni chinali392.
59Anthu ali mʼmunsiwa anabwera kuchokera ku mizinda ya Teli-Mela, Teli-Harisa, Kerubi, Adoni ndi Imeri, ngakhale samatha kutsimikiza kuti mafuko awo analidi Aisraeli enieni kapena ayi:
   60Zidzukulu za Delaya, zidzukulu za Tobiya, ndi zidzukulu za Nekoda. Onse pamodzi anali652.
61Ndi ena pakati pa ansembe anali awa:
Zidzukulu za
   Hobiya, Hakozi, ndi Barizilai (Zidzukulu za Hobiya, zidzukulu za Hakozi ndi zidzukulu za Barizilai. Barizilai ameneyu ndi uja anakwatira mmodzi mwa ana aakazi a Barizilai Mgiliyadi ndipo ankadziwika ndi dzina la bambo wawoyo.)
62Amenewa anafufuza mayina awo mʼbuku lofotokoza mbiri ya mafuko awo, koma mayinawo sanawapezemo, choncho anawachotsa pa unsembe ngati anthu odetsedwa pa zachipembedzo. 63Bwanamkubwa anawawuza anthuwo kuti asamadye nawo mpaka atapezeka wansembe wodziwa kuwombeza ndi Urimu ndi Tumimu.
64Chiwerengero cha anthu onse pamodzi chinali 42,360, 65kuwonjezera pamenepo, panalinso antchito awo aamuna ndi aakazi okwanira 7,337. Analinso ndi amuna ndi akazi oyimba nyimbo okwanira 200. 66Anali ndi akavalo 736, nyulu 245, 67ngamira 435 ndi abulu 6,720.
68Atafika ku Nyumba ya Yehova mu Yerusalemu, ena mwa atsogoleri a mabanja anapereka zopereka zaufulu zothandizira kumanganso Nyumba ya Mulungu pamalo pake pakale. 69Anapereka kwa msungichuma wa ntchitoyo molingana ndi mmene aliyense chuma chake chinalili: golide wa makilogalamu 500, siliva makilogalamu 2,800 ndi zovala za ansembe zokwanira 100.
70Ansembe, Alevi, oyimba nyimbo, alonda ndi antchito a ku Nyumba ya Yehova pamodzi ndi Aisraeli ena onse ankakhala mʼmidzi ya makolo awo.