Masalimo 117 (CCL)

Salimo 117
1Tamandani Yehova, inu anthu a mitundu yonse;
mulemekezeni Iye, inu mitundu ya anthu.
2Pakuti chikondi chake pa ife ndi chachikulu,
ndipo kukhulupirika kwa Yehova nʼkosatha.
Tamandani Yehova.